Mwalandilidwa pa Wikipedia, encyclopedia yaulere imene alionse anga thandizeni kukula! Pakali pano tili ndi nkhani zokwana 1,065 mu Chi-chewa, chinenero chomwe chimalankhulidwa ku Malawi ndi Zambia.
Za Wikipedia Wikipedia ya Chichewa ndi buku laulere. Ndi wiki, mtundu wa webusaiti yomwe anthu ambiri amawalemba. Izi zikutanthawuza kuti aliyense angathe kusintha tsamba lirilonse podalira pa "kusintha tsamba lino". Mungathe kuchita izi pa tsamba lirilonse losatetezedwa. Mukhoza kuona ngati tsambalo liri kutetezedwa chifukwa lidzati "View source" mmalo mwa "Sintha". Pali nkhani 1,065 pa Wikipedia ya Chichewa. Masamba onse ndi omasuka kugwiritsa ntchito. Zonse zafalitsidwa pansi pa Creative Commons Attribution / Share-Alike License 3.0 ndi GNU Free Documentation License. Mungathe kuthandiza pano! Mungasinthe masamba awa ndikupanga masamba atsopano. Werengani masamba othandizira ndi masamba ena abwino kuti mudziwe kulemba masamba apa. Ngati mukufuna thandizo, mukhoza kufunsa mafunso pachithumo cha Community. Mukamalemba nkhani apa Lembani masamba abwino. Masamba abwino kwambiri a encyclopedia ali ndi zothandiza, zolembedwa bwino. Osagwilitsa ntchito makina ngati google translator! Nkhani yolembedwa pogwilitsa ntchito translator wina aliyense siikhala yomveka bwino (Don't use machine translations!). Nkhani zotelo zizafufutidwa pano mopanda kudziwitsa olembayo komanso kupitiliza kutelo n'kuphwanya malamulo a Wikipediya. Gwiritsani ntchito masambawa kuti muphunzire ndi kuphunzitsa. Masambawa angathandize anthu kuphunzira Chichewa. Mutha kuigwiritsanso ntchito pangani Wikipedia yatsopano kuthandiza anthu ena. Khalani wolimba! Nkhani yanu siyenela kukhala yangwiro, chifukwa olemba ena adzakonza ndikupanga bwino. Ndipo chofunika kwambiri, musaope kuyamba ndi kupanga nkhani bwino.
Mu nkhani Luke Littler mu 2024 Luke Littler (womwe ali pachithunzi) wapambana PDC World Darts Championship. Wowombera mfuti ku Cetinje, Montenegro, akupha anthu 12 ndikuvulaza ena 4. Romania ndi Bulgaria akukhala mamembala athunthu a Schengen Area. Ku New Orleans, munthu wina wachiwembu analoza galimoto n’kufika pagulu la anthu n’kuyamba kuwombera, kupha anthu osachepera 14 ndi kuvulaza ena 35.
Chithunzi cha tsikulo
Wikipedia Muzinenero Zina
**Commons**Malo omwe aliyense angapeze ndikugawana zithunzi, makanema, ndi mawu aulere.